Proverbs 24

1Usachitire nsanje anthu oyipa,
usalakalake kuti uzikhala nawo,
2pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa,
ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.

3Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru,
ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;
4Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake
ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.

5Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri,
ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu.
6Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo.
Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo.

7Nzeru ndi chinthu chapatali kwambiri kwa chitsiru;
chilibe choti chiyankhule pabwalo la milandu pa chipata.

8Amene amakonzekera kuchita zoyipa
adzatchedwa mvundulamadzi.
9Kukonzekera kuchita za uchitsiru ndi tchimo,
ndipo munthu wonyoza amanyansa anthu.

10Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti
mphamvu yako ndi yochepadi!

11Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe;
uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa.
12Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,”
kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi?
Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi?
Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?

13Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino;
uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.
14Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako;
ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo,
ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.

15Usachite zachifwamba nyumba ya munthu wolungama ngati munthu woyipa.
Usachite nayo nkhondo nyumba yake;
16paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso.
Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.

17Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako.
Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.
18Kuopa kuti Yehova ataziona zimenezi nayipidwa nazo,
angaleke kukwiyira mdaniyo.

19Usavutike mtima chifukwa cha anthu ochita zoyipa
kapena kuchitira nsanje anthu oyipa,
20paja munthu woyipa alibe tsogolo.
Moyo wa anthu oyipa adzawuzimitsa ngati nyale.

21Mwana wanga, uziopa Yehova ndi mfumu,
ndipo usamagwirizana ndi anthu owachitira mwano,
22awiri amenewa amagwetsa tsoka mwadzidzidzi.
Ndani angadziwe mavuto amene angagwetse?

Malangizo Enanso a Anthu Anzeru

23Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa:

Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
24Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,”
anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
25Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino
ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.

26Woyankhula mawu owona
ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.

27Ugwiriretu ntchito zako zonse,
makamaka za ku munda
ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.

28Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa,
kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
29Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine;
ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”

30Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi
ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
31Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga,
mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa,
ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
32Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga
ndipo ndinatolapo phunziro ili:
33Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,”
kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
34umphawi udzafika pa iwe ngati mbala
ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.
Copyright information for NyaCCL